English to Chichewa Translation
English: The Environmental impact of any mining activity includes issues such as land use, waste management, water, air and soil pollution which are caused by the extraction, processing and the use of its products.
Chichewa: Zachilengedwe m`mene zimakhudzidwila ndi za migodi zimaphathikizaponkhani monga , kusewenzetsa nthaka ,kutsamira zinyalala ,madzi , mphweya ndiponso kuonongeka kwa nthaka. Ndipo dzimenezi zimachititsidwa ndi kuchotsa nzinthu m`nthaka , kudzipanga ndiponso kudzigwilitsira nchito.
English: We can’t wait for clean energy any longer. The future is green energy, sustainability & renewable energy. There is need for countries to invest in solar power/renewable and divert from fossil fuels.
Chichewa: Ife sithingathe kupitiliza kudikira mphamvu yoyera kwa nthawi yaitali. Koma tsogolo ndi lamphamvu zobiriwira, lokhadikika ndiponso la mphamvu zowonjedzereka. N`kofunika kuti maiko ayambe kutsunga ndalama ndi kuyamba kutsewenzetsa mphamvu ya dzuwa /kuwonjezereka ndiponso kusuntha ndi kuleka kusewenzetsa mafuta.
English: The legal and regulatory framework that governs the relationship between a host country government and investors in extractive industries is the backbone of long term investor-government relationship. The framework could include several pieces of domestic legislation (including the constitution, mining code, the tax law).
Chichewa: Malamulo ndiponso ndondomeko yoyendetsera zinthu imene imalamulira ubale wa pakati pa boma la dziko lolamulila ndi osunga ndalama m`mafakitale owonjezera ndiwo chiyambi cha mgwilizano wokhalitsa pakati pa boma ndi osunga ndalama. Ndipo zimenezi zikodzanso kuthandidza pa malamulo a mdzikolo.( kuphathikidzapo , malamulo ,ndondomeko ya zamigodi ndi lamulo la msonkho ).
English: Zambia has acceded to over 20 international environmental conventions, and these have a bearing on natural resource management. Different conventions are at different levels of domestication and implementation. Zambia lacks a well informed and organized local public sector to participate in publicizing the vulnerability of the environment and inculcating a sense of responsibility for the environment.
Chichewa: Zambia yakhala ikugwilidzana ndi maiko ena pa mitsonkhano yopotsa 20 yodzungulira zachilengedwe. Ndipo zimenezi zimakhudzanso kutsamalira zachilengedwe. Mitsonkhano imeneyi ili m`magulu osiyana-siyana a pakhomo ndi kukhadzikitsidwa kwake. Zambia ilibe gawo lodziwika bwino ndiponso lokonzedwa bwino lomwe imagwila nchito kufalitsa za chiopsedzo pa chilengedwe ndiponso kuphunzitsa anthu kukhala ndi udindo pa nkhani ya zachilengedwe